Akaniza belo, DNA kwa a Malemia

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 05 May 2026
📘 Source: MWNation

Bwalo la milandu ku Zomba lakana kupereka belo kwa Senior Chief Malemia komanso kuyeza DNA kuti adziwe mimba imene mfumuyo idathandizira mtsikanayo kuchotsa idali ya ndani. Woweruza a Elijah Daniels adauza bwalolo kuti lakana kupereka belo chifukwa zichedwetsa kumaliza mlanduwo. Kuchokera pa 25 March pamene mfumuyo, imene dzina lawo la pa msonkho ndi Clement Lloyd idamangidwa, kameneka ndi kachitatu kukanidwa belo.

Malinga ndi chigamulo chimene bwalolo lidapereka pa 7 April chaka chino, mfumuyo idapezeka ndi milandu iwiri: Wogonana ndi mtsikana wachichepere komanso kuthandizira kuchotsa mimba. Ndipo a Daniels adakana pempho la woimira mfumuyo a Patrick Debwe kuti pasayezedwe DNA chifukwa milandu akuyankhayo palibepo wofufuza kuti mimbayo ndi ya ndani. “Ndondomeko zoyeza DNA zikhonza kuchedwetsa mlandu,” adatero iwo. Bwalolo lapereka mwayi kwa woimirira mfumuyo kuti akhonza kukachita apilo zimene bwalolo lagamula ndipo mlanduwo udzalowanso pa 5 May 2026 pamene a Debwe adzayambe kuteteza mfumuyo.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • May 05, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope