MRA ikuyendera nyumba za renti

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 08 March 2026
📘 Source: MWNation

Bungwe lotolera misonkho m’dziko lino la Malawi Revenue Authority (MRA) lati layamba kuyendera khomo ndi khomo anthu amene ali ndi nyumba m’mizinda ya Blantyre. Malinga ndi chikalata chimene wasainira ndi mkulu wa bungwelo a Felix Tambulasi, maofisala atatu kapena anayi akhala akupita m’maderawo ndi kutolera zinthu monga nambala ya puloti, mtundu wa nyumba, chaka chimene idamangidwa, kuchuluka kwa anthu m’deralo, pamalopo pa nyumba zingati za renti komanso ndalama zimene amatolera pa mwezi kuchokera kwa a renti. “Maofesala athu azivala zoonetsa kuti amagwira ntchito ku MRA komanso zitupa zawo ndipo adzakumana ndi a landilodi, woyang’anira nyumbayo komanso amene4 akudziwa bwino za nyumbayo.

Tikupempha kuti anthu onse azifunsa ogwira ntchitoyo kuti aonetse zowazindikiritsa,” atero a Tambulasi. Malinga ndi mmodzi mwa akuluakulu a MRA Mayi Wilma Chalulu, kutolera zofunikazi kuthandizira bungwelo pomwe liyambe ntchito yotolera misonkho pa nyumba za renti. “Gawo 11 la malamulo oyendetsa za misonkho likupereka mphamvu kwa MRA kutolera misonkho kuti njira iliyonse imene m’Malawi amapezera ndalama, boma liyenera kutolerapo msonkho,” adatero iwo.

Aphungu a Malamulo adavomereza bilu yosintha malamulo a misonkho kuti MRA izitoleranso misonkho ina, kuphatikizapo pa ndalama zopezeka polipira renti. Aphungu 94 ndiwo adavotera kuti biluyo idutse, pomwe 49 adakana ndipo awiri adajomba. Mmodzi mwa eni nyumba mu mzinda wa Lilongwe wati nkhaniyi siyowawa kwa eni nyumba koma matenanti chifukwa malandilodi akweza nyumba mosalingalira matenanti.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

“Zimenezi zingochititsa kuti mitengo ya lendi ikwere komanso mpomwe anthu alimve kuwawa dziko chifukwa moyo ulimba,” watero mwini nyumbayo. Koma mosemphana naye pang’ono, tenanti wina wati zitengera umunthu wa eni nyumba chifukwa akuyenera kulingalira iwowo ali tenanti. “Apapa eni nyumba akakwenza lendi zingopangitsa kuti nyumba zambiri zikhale zopanda anthu,” watero tenantiyo.

Zomwe wanena tenantiyo zidayamba kale kuoneka makamaka mu mzinda wa Lilongwe momwe matenanti ambiri akusaka nyumba zotsika mtengo. Ndipo mkulu wina wochita bizinesi ya zootcherera ku Zomba wati kubwera kwa misonkhoyo kuchititsa kuti apite azikakhala m’madera a ku midzi.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • March 08, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope