Anthu okhala mozungulira, komanso pa zisumbu m’nyanja ya Malawi; pamodzi ndi ochita malonda osiyanasiyana akuyembekezera ndi chidwi kupherezera kwa lingaliro la boma lokhazikitsa sitima zinayi zatsopano pa nyanjayi. Chiyembekezochi chikudza polingalira zipsinjo zomwe zakhala zilipo kwa nthawi yaitali monga kusadalirika, komanso chiopsezo cha ngozi pa maulendo a pa nyanja zomwe sitima zatsopanozo zikuyembekezeka kudzathetsa pambali pokweza ntchito za malonda makamaka ndi maiko oyandikana nawo. Masiku apitawa, unduna woona za mtengatenga ndi mtokoma lidasainirana mgwirizano ndi kampani ya Xiao Xiang Investment ya ku China kuti ikonze sitima ziwiri zonyamula katundu, imodzi yonyamula mafuta ndi inanso yonyamula anthu; komanso kukonza madoko a Chipoka ku Salima ndi Kaporo m’boma la Karonga.
Ngakhale mbali ziwirizi sizidaulule ndalama zogwirira ntchitozi, mgwirizanowu ukutsimikizira chidwi chomwe chakhala chikusowa kumbali ya boma pa nkhani yokweza ntchito za mtengatenga makamaka wa pamadzi m’zaka zochuluka. Kupatula kupumitsa sitima ya MV Ilala yomwe yakhala ikuyenda pa nyanja ya Malawi kwa zaka 75, ntchito yopanga sitima zatsopano ndi yokonza madoko awiriwo zidzachititsa nyanjayo kukhala mpita wodalirika pa nkhani za mtengatenga, komanso kuchepetsa mlingo wa katundu yemwe amayenda pa misewu ya m’dziko muno. Mlembi wamkulu ku unduna woona za mtengatenga a Bright Kumwembe adati: “Mitengo ya maulendo, komanso yonyamulira katundu ikuyembekezeka kudzatsika sitima zinazo pamodzi ndi madoko awiriwo zikadzayamba kugwira ntchito.
Tikuyembekezeranso kuti ntchito za mtengatenga, komanso malonda pakati pa dziko lino ndi oyandikana nawo zidzapitanso patsogolo.” Malingana ndi a Kumwembe, imodzi mwa sitima zatsopanozo ikuyembekezeka kuyamba kugwira ntchito m’miyezi 12 ikudzayi ndipo kupatula kuchepetsa kudalira kwambiri mayendedwe a pa msewu zidzachititsa kuti zokolola ndi katundu wina monga fetereza ndi mafuta a galimoto zizifika mosavuta m’dziko muno ngakhalenso kuzitumiza maiko ena. Nyanja ya Malawi njotalika makilomita pafupifupi 580 ndipo phindu lokhazikitsa sitima za makonozo lidzafikira asodzi ndi alimi ochuluka kuyamba kutumiza nsomba ndi zokolola zawo m’madera ena akutali mosavuta. Nazo ntchito zokopa alendo ndi bizinezi zikuluzikulu zikuyembekezeka kudzapita patsogolo zedi.
[paywall]
“Tikuyembekezera kuti katundu monga zokolola zakumunda zizidzayenda mwa changu ndi motsika mtengo zomwe zidzachititsa kuti ndalama zochitira bizinesi pa msika zidzakhalenso zochepa,” adatero mtsogoleri wa bungwe la anthu ogula ndi kugulitsa mbeu m’dziko muno, a Grace Mijiga, popereka ndemanga yake. “Tikukhulupilira kuti boma lidzakhazikitsanso malo abwino ndi odalirika osungira katundu ku madoko a Kaporo ndi Chipoka, komanso kuti katundu azidzakwezedwa ndi kutsitsidwa m’sitima mosavuta ndi motetezeka ngakhale atachuluka motani,” a Mijiga anaonjezera motero. Madoko awiriwa ndi gawo lofunika kwambiri lolumikizitsa mayendedwe a pa nyanja, pa njanji ndi pa msewu, komanso kuteteza misewu yambiri yomwe yakhala ikuonongeka pafupipafupi kaamba konyamula katundu wochuluka mowirikiza.
Mtsogoleri wa gulu la eni kampani zothandizira kulowetsa katundu wa kunja m’dziko muno, a Yohane Kapalamula ati kukula kwa chiwerengero cha anthu ndi katundu oyenda pa sitima za pamadzi m’malo mwa pa galimoto kudzathandiza kutukula ntchito za mtengatenga m’dziko muno. “Msewu wathu wa M1 udzapeputsidwa ndi kukhala wa ngwiro, komanso mtengo woitanitsira katundu monga mafuta a galimoto ndi zipangizo za ulimi udzatsikirapo. Kuonjezera apo, madera osiyanasiyana a mphepete mwa nyanja adzakhala olumikizika mosavuta,” adatero a Yohane. Iwo adatsindika kuti kupambana kwa lingaliroli kwagona pokhala ndi madoko odalirika, misewu yabwino yolowera ndi kutuluka ku madokowo, kukonza ndi kusamalira sitimazo mowirikiza, komanso kupezeka kwa katundu woti azinyamulidwa pa sitimazo.
[/paywall]
All Zim News – Bringing you the latest news and updates.