Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 02 June 2026
📘 Source: Malawi 24

Mtsogoleri wa dziko lino, Arthur Peter Mutharika wati salola mphekesera kapena nkhani zopekedwa pazifukwa za ndale kuti zisinthe chidwi cha boma lake chofuna kubwezeretsa chuma cha dziko lino mchimake. Mawu a Mutharika akudza kutsatira mafunso omwe anthu akufunsa makamaka pa masamba a mchezo kuti ndichifukwa chani mtsogoleri wa dziko linoyu sanapezeke ndikutsogolera mkumano wa nduna omwe unalipo sabata yatha. Kuwonjezera apo, izi zikubwera pomwe anthu ena akupenekera kuti ubale wa Mutharika ndi achiwiri ake, Jane Ansah ndi Enock Chihana suli bwino pomwe anthu akudabwa kuti bwanji m’tsogoleri wadzikoyu sakumawatuma awiriwa kukamuyimirira ku zochitika zosiyanasiyana.

Nthawi zonse, Mutharika akamatuma nduna zake kukamuyimirira ku zochitika zosiyanasiyana osati achiwiri akewa, zomwe zabweretsa manong’onong’owa. Koma poyankha mphekeserazi kudzera mukalata yomwe wasainira ndi mlembi wa mkulu wa boma, Justin Saidi, Mutharika wati zonsezi ndi bodza pa mnkhuniza ndipo wati salola kuti nkhani zabodza ngati izi zimuthawitsire chidwi chake chofuna kukoza mavuto omwe akuta dziko lino. “Pulezidenti nthawi zonse wakhala akunena momveka bwino kuti cholinga chake chachikulu ndi kuthana ndi mavuto azachuma mdziko muno, kulimbitsa ntchito komaso kuthana ndi njala.

Iye chidwi chake chidakali pa ntchitoyi ndipo salola kusokonezedwa ndi mphekesera kapena mabodza,” yatero kalatayo. Mutharika wati akumatuma nduna ku zochitika osati achiwiri ake ngati imodzi mwa njira zothandizira kuchepetsa ndalama zomwe boma limagwiritsa ntchito, ndipo wanenetsa kuti ubale wake ndi achiwiri ake onse uli khethekhethe ngati chitseko ndi feremu. “Zisankho zotere sizikumachitika chifukwa cha njiru, kapena udani uli onse, koma cholinga chake ndi kulimbikitsa ulamuliro wabwino, kuchepetsa ndalama zomwe boma limagwiritsa ntchito,” wateloso Mutharika kudzera mukalatayo.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on Malawi 24

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Mutharika watsimikizira a Malawi kuti boma lake lipitirirabe kudzipereka pochitira zinthu poyera, kutukula chuma cha dziko lino, komaso kuwonetsetsa kuti a Malawi akusamalidwa bwino. This site uses Akismet to reduce spam.Learn how your comment data is processed.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by Malawi 24 • June 02, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope