Otsutsa aopseza kunyanyala zokambirana atamangidwa

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 07 February 2026
📘 Source: MWNation

Aphungu otsutsa boma ku Nyumba ya Malamulo aopseza kuti zomanga aphungu mwachisawawa zikapitirira iwo a zinyanyala ntchito za ku nyumbayo chifukwa pena boma likuphwanya malamulo. Aphunguwo motsogozedwa ndi mkulu wambali yotsutsa a Simplex Chithyola Banda adakumana ndi sipikala wa nyumbayo a Sameer Suleman Lolemba kuwadandaulira kuti aphungu ena akumangidwa pomwe makomiti a limkat i mokumana. A Chithyola Banda adati zomwe zikuchitikazo nzosayenera pa malamulo ndipo adati zikapanda kusintha , aphungu otsu t sa makamaka achipani cha MCP azinyanyala za ku nyumbayo.

“Sitingangokhala ngati kuti palibe chomwe chikusokonekera, malamulo tikuwadziwa ndipo amanena kuti phungu sayenera kumangidwa pomwe akupita, kuchokera kapena alimkat i mwazochitika za ku Nyumba ya Malamulo,” adatero a Chithyola Banda. Izi zikuchitika pomwe mtsogoleri wa dz iko lino a Peter Mutharika akuyembekezeka kudzatsegulira mkumano wa aphungu Lachisanu l i k u b w e r a l i k u t i akakambirane bajet i ya 2026-2027. Aphunguwo asadafike apa, ofesi ya Nyumba ya Malamulo idali italembera kale kalata mkulu wapolisi a R i c h a r d L u h a n g a kuwakumbutsa zomwe malamulo achitetezo cha aphungu amanena.

“Monga mukudziwa , makomiti osiyanasiyana a ku Nyumba ya Malamulo akukumana ndiye pa nyengo yotere, aphungu amakhala o t e t e z edwa k u f i k i r a atamaliza zokambirana zawo ndipo atabwerera kwawo,” idatero kalatayo. K oma a L u h a n g a adati: “Nkhanizi zili ku mabwalo a milandu ndiye sindingayankhe kanthu padakalipano.” Nkhani yonse ikukhudza kumangidwa kwa aphungu a MCP anayi ndi phungu wa chipani chomwecho koma wodziimira payekha m’Nyumba ya Malamulo a Vitumb i ko Mumba woyimira Mzimba Central. Aphungu ena ndi a Ri c h a rd Chimwendo a Dowa East, a Moses K u n k u y u a D e d z a Mlunduni, a Sam Kawale a Dowa North East ndi a Sosten Gwengwe a Lilongwe Msozi North.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

P o l a n k h u l a n d i atolankhani Lachitatu k u L i l o n g we , g u l u l o t c h e dwa Mb a dwa zokhudzidwa lidati a ndale amangofuna kuzunzana n d i m c h i t i d w e w u koma milandu yomwe amatengerana imafera m’malele. “Si tidaonepo pomwe p ama t h e r a n k h a n i zimenezi, amangozunzana n’ kumaononga ndalama za boma. Mwa chitsanzo pa milandu yomwe boma la MCP l i d amang i r a akuluakulu a DPP ili pati?” adatero mtsogoleri wagululo a Fredrick Malata.

Iwo adati mpofunika kulondol oz a m i l andu yo n s e k u t i Ama l awi a z i d z i w a m o m w e ikuyendera chifukwa pena imangobwezera chitukuko mmbuyo poti ena mwa omangidwawo amakhala kuti panthawiyo amafunika pa chitukuko china chake. Iwo adadabwanso kuti m’mwezi wa December 2021, mt sogol e r i wa DPP Peter Mutharika ali kotsutsa adapempha a Lazarus Chakwera omwe adali pulezidenti kuti boma lisiye kumanga akuluakulu a chipani cha DPP koma pano pomwe a Mutharika a li m’ boma akupanga zomwezo.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • February 07, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope