Bwalo la milandu la Zomba Senior Resident Magistrates Court kuyambira 8 koloko mawa lino lipitiriza kumva mlandu wa a Senior Chief Malemia omwe akuwaganizira kuti adagona ndi mtsikana wa zaka 16 n’kumupatsa mimba kenako n’kumuchotsetsa. Izi ndi malingana ndi zikalata za bwalo zimene taona zimene zikusonyeza kuti mlanduwo akufuna kuti uyende mwachangu, kaamba koti woganiziridwawo sadatulutsidwe pa belo. Malinga ndi zikalatazo, bwalo likufuna kumalizitsa kumva umboni ngakhale lero ndi mawa lomwe ndi tsiku la tchuti mpaka mkuja.
Izi zikudza pomwe woweruza mlanduwo a Elijah Daniels Lachitatu sabata yatha adauimika kaye chifukwa choti pomwe woimira mfumuyo pa milandu a Patrick Debwe amafunsa mayi a mwanayo mafunso atapereka umboni wawo nthawi yoweruka ya boma 4:30pm idali itakwana ndipo bwalolo lidaonjezera nthawi mpaka 5pm. Koma a Debwe, omwe amagwira ku kampani ya Chimowa and Associates Law Consultants, adali asadamalize kotero bwalolo lidaimitsidwa kuti adzapitiriza kufunsa mayiwo pa tsiku loikikalo. Mfumuyo, yomwe dzina la pa msonkho ndi a Lloyd Clement ndipo ali ndi zaka 33, itaonekera ku khotilo Lachitatu, mtsikanayo adaperekera umboniwo m’kachipinda komata kaamba koti ayenera kutetezedwa pokhala wachichepere.
Ndipo popereka umboni wawo, mayi a mtsikanayo amene ndi a zaka 50, adati adayamba kumukaikira mwezi wa December chaka chatha kuti adali ndi mimba koma akamufunsa amakana. Iwo adati chifukwa amakhala pafupi ndi a mfumu woganiziridwawo, adakawauza akazi awo kuti awathandizire kufunsa mwanayo ngati ali ndi mimba kapena ayi. Atamufunsa adavomera.
[paywall]
“Koma atamufunsa kuti mimbayo adamupatsa ndani, adayankha kuti zimenezo zisawakhudze. Mmawa wa pa 26 February mtsikanayo adayamba kuonetsa zizindikiro zoti akudwala koma pomufunsa, adakana,” adatero iwo. Malinga ndi mayiwo, adapitanso kwa mkazi wa mfumuyo kukawauza zizindikiro zimene mtsikanayo amaonetsa.
Iwo adati mayi mfumuwo adati dzulo lake adamuona akukwera minibasi atanyamula ka chikwama kakang’ono. Mayiyo atabwerera ku nyumba kwawo, adati adapeza mtsikanayo ali mu ululu ndipo atatsegula kachikwamako adapeza kapaketi ka mankhwala koma mulibemo mapilitsi. Ndipo adapezamonso lisiti lomwe adagulira mankhwalawo.
“M’ma 2 koloko masana, matenda adakulirabe ndipo adawauzanso akazi awo a mfumuwo awaperekeze ku chipatala cha St Lukes m’bomalo. Madokotala atamufunsa adayankha kuti adamwadi mankhwalawo m’ma 8 koloko mmawa ndipo atamufunsa kuti mankhwalawo adawatenga kuti adayankha kuti kwa chibwezi chake,” adatero mayiyo. Ndipo adapitiriza kuti madotolowo adawafunsanso ngati mtsikanayo adali atayamba kale sikelo.
Pakati pa usiku, mtsikanayo adabereka senye. Mayiyo adapereka ku bwalolo ka bokosi ka mankhwalako ndi lisitiyo ngati umboni.
[/paywall]
All Zim News – Bringing you the latest news and updates.