Kampeni itha mawa

Mar 14, 2026
Kampeni itha mawa

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 14 March 2026
📘 Source: MWNation

Pomwe Chisankho Chapadera chikuchitika m’madera a aphungu 4 ndi makhansala 9 Lachiwiri, kampeni yovomerezeka imene idayamba pa 15 January itha mawa. Bungwe la zisankho la MEC lichititsa chisankhocho m’madera a aphungu a pakati ku Rumphi, ku Nkhotakota Liwaladzi, Dedza Mtakataka ndi kumadzulo kwa boma la Blantyre. Chisankho cha makhansala chilipo ku Ighembe m’boma la Karonga, Luwinga mu mzinda wa Mzuzu, Linthembwe ku Dowa, Msitu ku Mchinji, Mikongo ku Mangochi, Chanda ndi Chirunga ku Zomba komanso ku Muonekera m’boma la Thyolo.

Kuli mkokemkoke pamene anthu 26 adzapikisane nawo pofuna mpando wa phungu ndipo chipani cha DPP chokha ndi chimene chili ndi ochiimirira m’madera onse 4 pomwe chipani cha MCP chilibe wochiimirira ku Muonekera. Chipani cha Aford chikuimira m’madera awiri pomwe zipani za UTM, PDP ndi PPM zili ndi ofuna uphungu mmodzimmodzi pomwe anthu 14 akuima pa okha. Kumbali ya makhansala, chipani cha DPP chikuimiranso m’madera onse 9 pomwe MCP ili ndi madera 6 motsagana ndi UTM (4), Aford (3) ndipo NDP, Petra, MRP, UDF, MRP komanso Odya Zake ali ndi khansala mmodzimmodzi pomwe anthu 27 akuima pa okha.

Pali amayi 11 amene akufuna uphungu ndi enanso 11 amene akufuna ukhansala. Achinyamata awiri, Thokozire Lunji wa DPP ku Liwaladzi ndi Turson Kaliza wa DPP kumadzulo kwa Blantyre ndiwo akupikisana nawo pa mpando wa uphungu. Munthu mmodzi yekha, a Lackson Jagaja omwe akuimira ku wodi ya Mikongo, ndiwo ali aulumali okhawo amene akupikisana nawo pa chisankhochi.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Polankhula ndi mtolankhani wathu Lachitatu pa mtsutso umene bungwe lophunzitsa anthu zosiyanasiyana la Nice lidakonza mwa agulupu a Matenganya ku Mikongo, a Jagaji adali ndi chikoka kwambiri kaamba ka mfundo zawo zachitukuko. “Ine ndikuima nawo chifukwa ndikufuna kutukula miyoyo ya anthu a ulumali ndi kupititsa patsogolo chitukuko mu wodiyi. Ndikuimira nawo chifukwa miyoyo ya anthu amene ali ndi ulumali ikukhala yovuta,” adatero iwo.

Ndipo adanenetsa kuti adzaonetsetsa m’deralo muli misewu yabwino, zipatala, madzi aukhondo ndi zofunikira zina. Iwo akupikisana ndi Mayi Aisha Chikoloni, a James Royd ndi a Lackson Simba amenenso akuima pa okha komanso Mayi Ruth Makwinjaamene akuimira UDF. Ndipo zokonzekera chisankhochi zakhala zikuyenda bwino ngakhale pakhala zotsamwitsa apa ndi apo.

Mkulu woyendetsa chisankho m’boma la Nkhotakota a Nickson Chimangeni adati ndi wokonzeka kuyendetsa chisankho ku Liwaladzi ngakhale kuti ino ndi nthawi ya mvula pomwe madera ena amakhala ovuta kufikako monga Katimbira, Chiphole, Chauma, Chipungu ndi Khonde. “Madera ena ndi ovuta kufika makamaka ndi mvulayi koma mothandizana ndi komishoni ya MEC zonse zitheka ndithu. Tikuonetsetsa kuti kampeni iyende mopanda ziwawa komanso kuti opikisana onse akutsatira malamulo,” adatero iwo.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • March 14, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope