Zina ukamva kamba anga Mwala, zaphelezera m’boma la Nkhotakota pomwe anthu agwira Kadzidzi wa chilendo mnyumba atanyamula Kalata za uthenga othetsa banja m’mudzi mwa Phangwa m’bomalo. Malinga ndi uthenga omwe tapeza ati Kadzidziyo anapezeka atanyamula kalata ziwiri zonyamula uthenga opita kwa Mayi wa m’nyumbamo. Uthenga wa mkalatazo watsindika kuti banja lithe ponena kuti mkazi wa bambo wa mnyumbamo amulekele mwamuna wake, yemwe dzina lake ndi Thom.
kadzidziyo anasenza uthenga wa chidule kuti “Undipatse mwamuna wanga” komanso kalata ina yati “Iwe Thom ndabwera ine, tiye tidzipita ntchito tikugwilira limodzi.” zomwe zachitikazi zazizilitsa anthu nkhongono ponena kuti zifukwa za zodabwitsazi sizikudziwika ndipo apolisi akwanitsa kunyamula kadzidziyo limodzi ndi makalata omwe anali nawo komanso kukhazikitsa bata mderalo. Paul Malimwe, mneneli wa apolisi m’boma la Nkhotakota sadayankhulebe pa nkhaniyi.
Read Full Article on Malawi 24
All Zim News – Bringing you the latest news and updates.