‘Chuma chifike kumudzi’

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 28 February 2026
📘 Source: MWNation

Nduna ya za chuma a Joseph Mwanamvekha ati ndondomeko ya za chuma imene apereka m’Nyumba ya Malamulo dzulo ikuonetsetsa kuti chuma chochoka ku thumba la boma chizifikadi kwa Amalawi akumudzi. Boma likuyembekezera kugwiritsa ntchito K10.978 triliyoni kuyambira chaka chino mpaka chaka cha mawa. M’bajetiyo, a Mwanamvekha adati boma lachilimika poika ndalama zochuluka ku za ulimi, zikopa alendo, za migodi ndi mafakitale.

Ku nkhani ya za ulimi kulowa K931 biliyoni pomwe zokopa alendo ndi mafakitale kupita K51.2 biliyoni pomwe za mphamvu ndi migodi kulowa K352 biliyoni. Pa nkhani ya maphunziro, boma ligwiritsa ntchito K1.28 triliyoni, pomwe za umoyo kulowa K1.02 triliyoni. Nkhani ya za mtengatenga ndi mtokoma kulowa K664.3 biliyoni.

Ku thumba la chitukuko la CDF kulowa K1.45 triliyoni. Polankhula ndi atolankhani atapereka ndondomeko ya momwe boma ligwiritsire ntchito chuma chake chaka chino mpaka chaka cha mawa, a Mwanamvekha anati bajetiyo aikonza moti chuma chiyambenso kuyenda bwino. Iwo anati chachikulu n’choti Amalawi nawo azitha kuchita mapulani pa momwe zikuyendera pa nkhani ya chuma pakhomo.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

“Tikufuna kukonza chuma chathu kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino. Komanso tikufuna Amalawi ayambe kupanga pulani chifukwa kayendetsedwe ka chuma kakhazikika. Tionetsetsanso kuti ndalama zichoke ku thumba la boma ku Lilongwe zipite kumudzi komwe zikagwire ntchito ya chitukuko,” atero a Mwanamvekha.

Iwo adati izi zikusiyana ndi mmbuyomu pomwe ‘ndalama zimangopita ndi kumangodyedwa, osati kugwiritsa ntchito njira zosakhala za chitukuko’. “Komanso taonetsetsa kuti makampani amene akupanga zinthu m’Malawi muno tiwateteze kuti azitha kupanga zinthuzo mosavuta. Tikufuna kulimbikitsa kuti tizitumiza zinthu kunja,” adatero a Mwanamvekha.

Ndipo adaonjeza kuti mitengo ya zinthu ikuyenera kukhala yokhazikika. Chiongola dzanja Amalawi akatenga ngongole chisakhale chokwera. A Mwanamvekha adapereka bajeti ya K10.98 triliyoni ndi cholinga chachikulu choti ndalama zimene boma limapeza ndi zomwe limagwiritsa ntchito zisasiyane kwambiri.

Bajetiyo ikuyesetsanso kuti boma lizitolera ndalama zochuluka komanso kuyesetsa kuti boma libwenze ngongole zimene lili nazo. Koma mkulu wa zipani zotsutsa boma a Simplex Chithyola Banda adati bajeti imene apereka a Mwanamvekha siikupereka chiyembekezo kwa Amalawi makamaka chifukwa misonkho yankitsa. Polankhula ndi mtolankhani wathu, a Chithyola Banda adati misonkho yachuluka moti ogwira ntchito m’boma akupita n’kochepa ku nyumba.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • February 28, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope