Chimanga ‘amachibisa’ chatuluka

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 31 January 2026
📘 Source: MWNation

Patangotha masiku ochepa boma litayamba kulandira chimanga chomwe lagula m’dziko la Zambia, mavenda nawo atulutsa chimanga chawo chomwe akufuna kukagulitsa ku misika ya Admarc ndi nkhokwe za boma za NFRA. Izi zautsa manong’onong’o woti mavenda ena amabisa dala chimangacho poyesa kuti chidzakwera mtengo ndipo adzapange ndalama zambiri pogulitsa. Malingana ndi nduna ya za malimidwe Mayi Roza Mbirizi, mavenda adagula chimanga chambiri ndipo mmalo mochigulitsa, ankangochisunga pomwe anthu amalira ndi njala.

“Chimanga chidalipo ndipo umboni wake waoneka pomwe galimoto za mtengatenga zandanda m’misewu kufuna kukagulitsa chimanga. Kumeneku n’kusokoneza mapulani aboma,” atero a Mbirizi. Kuyenda m’misewu ina mu mzinda wa Lilongwe kukuvuta kaamba koti galimotozo zayalana kulowera ku misika ya Admarc.

Mkulu wa bungwe la Malawi Agricultural Policy Advancement and Transformation Agenda (Mwapata) Institute a William Chadza ati mpofunika kuti boma lizikhala ndi njira zoti chimanga chisamasowe pa msika. Iwo ati n’zodabwitsa kuti pompano mbiri idali yoti chimanga kulibe koma chitangoyamba kufika chochokera ku Zambia, amalonda a m’Malawi nawo akhamukira ku msika. “Apapa zikuonetsa kuti pali kagulu kena kake komwe kamati alimi akamakolola kamagula chimanga limodzi ndi mbewu zina n’kubisa.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Koma zimenezi n’zofunika njira yozithetsera,” atero a Chadza. Boma lidagula matani 200 000 m’dziko la Zambia kuti lisokelele pomwe pamaperewera malipoti atasonyeza kuti anthu oposa 4 miliyoni asowa chakudya pakati pa miyezi ya November 2025 ndi April 2026. A NFRA atalengeza kuti ayamba kugula chimanga pa mtengo wa K55 000 pa thumba la makilogalamu 50, mavenda ambiri akuthamangira kokagulitsa kuopa kuti mtengowo ungagwenso.

Wogwirizira mpando wa za kafukufuku ku bungwe la National Planning Commission (NPC) a Andrew Jamali adati mpofunika kukhala ndi njira yolondolozera zokolola ndi momwe zikugwira ntchito. “Ngati dziko tikuyenera kumadziwa kuti zokolola zathu zikuyenda bwanji chifukwa tikhonza kumangodandaula chonsecho tili ndi zokwanira. Komanso boma lizitha kuteteza chimanga kuti chisamatuluke wamba,” atero a Jamali.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • January 31, 2026

Powered by
AllZimNews

By Hope