Katswiri womwetsa zigoli ku timu ya Mighty Wanderers Muhammad Sulumba wazaka 31, walonjeza kuti chaka chino awonetsa anthu kuti akanali ka mwana, pomwe wakonzekera kulanga ma timu.Poyankhula ndi tsamba la Wa Ganyu, Sulumba wati ngakhale ena amamunena kuti ndi nkhalamba, chomwe amadziwa ndichoti iye akanali wachichepere ndipo ali ndi nthawi yochita zinthu zazikulu pa masewera a mpira wamiyendo.“Ma timu ndiwapweteka ndipo inuyo mudzachitira umboni” watero Sulumba powachenjeza ma timu. “Ndine mwana ngakhale amandinena kuti nkhalamba ndipo izi zimachitika ku Malawi kokha kuno pomwe kunja anthu amasewera nthawi yayitali.”Katswiriyu watiso ali ndi masomphenya okaseweraso mpira kumaiko akunja, zomwe watsimikiza kuti izi zichitikadi.“Luso langa silikuthera ku Wanderers komweku, ndikuyang’ana kupita chitsogolo.
Ndipemphero langa kuti nditulukeso kukasewera kunja ndipo izi zitheka potengeraso ndi zintchito zomwe ndiwonetse chaka chino”Katswiriyu anayamba kusewera ligi yayikulu mdziko muno ku timu yomwe inkatchedwa Blantyre United mu 2012 pomwe anali ndi zaka 16.Chaka chotsatira anapita ku Mighty Wanderers kenaka mu 2016 analowera ku timu ya Nyasa Big Bullets.Katswiriyu waseweraso ma timu akunja kwa dziko lino monga Polokwane City yaku South Africa komaso ena atatu kumaiko a Aluya.Asanabwerere ku Wanderers, Sulumba waseweraposo Ma timu a mdziko muno monga Civo Service United komaso CRECK Sporting Club. This site uses Akismet to reduce spam.Learn how your comment data is processed.
Read Full Article on Malawi 24
All Zim News – Bringing you the latest news and updates.