Boma lapereka K100biliyoni yogulira chimanga

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 27 July 2026
📘 Source: MWNation

Nduna ya za chuma, mapulani a za chuma, komanso kupereka mphamvu ku anthu a Joseph Mwanamvekha yati boma lapereka K100 biliyoni zogulira chimanga ku nthambi ya National Food Reserve Agency (NFRA). Poyankhula m’Nyumba ya Malamulo mkati mwa sabatayi, a Mwanamvekha anati ndalamazo ndi gawo la ntchito yolimbikitsa chitetezo cha chakudya m’dziko muno pamene akatswiri akulosera za nyengo ya El Niño yomwe imapereka chiopsezo ku ntchito za ulimi. Malingana ndi ndunayo, cholinga cha ndalamazo n’kufulumizitsira ntchito yogula chimanga kwa alimi m’madera kuti nkhokwe za boma zikhale zodzala bwino pofuna kuteteza Amalawi ku njala yomwe ingadze kaamba ka kuchepa kwa zokolola.

“Nditsimikizire Nyumba yolemekezekayi kuti mmene ndikuyankhulamu, nthambi ya NFRA ili kale ndi chimanga m’nkhokwe zake, china chochokera ku Zambia, komanso tapereka K100 biliyoni ku nthambiyi kuti igule chimanga china choonjezera,” adatero a Mwanamvekha. Ndunayi idatinso nthambi yoona zogula ndi kugulitsa katundu wa boma ya Public Procurement and Disposal of Assets Authority (PPDA) idapereka chilolezo ku NFRA kupitiriza ndi ntchito yogula chimanga itaunikira ndondomeko zonse zokhudza dongosololi. Komabe, a Mwanamvekha sadafotokoze chifukwa chomwe unduna wake waperekera K100 biliyoni pomwe ndondomeko yoyendetsera chuma cha boma ya chaka cha 2026/27 idapatula K60 biliyoni yokha kuti NFRA igulire chimanga.

Mkulu wa NFRA a Bruce Munthali adauza Tamvani kuti nthambiyi yalandira kale K20 biliyoni ndipo ikuyembekezera kuyamba kulandira chimanga potsatira mapangano omwe yachita ndi ogulitsa osachepera 185. Iwo adati K100 biliyoni yomwe NFRA yalandira ithandiza kugula matani 108 000 a chimanga pa mtengo wa K900 pa kilogalamu womwe boma lidakhazikitsa. “PPDA idatipatsa chilolezo kuti tikhoza kupereka makontalakiti omwe timayenera kupereka ndipo ndine wokondwa kuti tapereka kale makontalakiti 185 kwa ogulitsa omwe adakwaniritsa ndondomeko,” adatero a Munthali.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Iwo adatinso kuphatikiza pa matani 62 000 omwe NFRA ili nawo kale, chimanga chomwe nthambiyi ikuyembekezera kugula chidzafikitsa mlingo wa m’nkhokwe zake pa matani pafupifupi 170 000. Komabe, a Munthali adavomereza kuti mlingowu ukhalabe wotsika ndi matani 47 000 poyerekeza ndi mlingo wa matani 217 000 womwe ndi woyenera. Iwo adati boma likusakasaka njira zina zopezera ndalama kuphatikiza kukambirana ndi abwenzi ake osiyanasiyana kuti chimanga choonjezera chipezeke pofuna kupewa mavuto omwe angadze kaamba ka nyengo ya El Niño.

Chitsimikizo cha ndalamazi chidabwera potsatira nkhawa ya phungu wa dera la Dedza Mphunzi a Emmanuel Mawindo atadandaula za kuchedwa kwa nthambi ya NFRA ndi kampani ya Admarc Ltd kuyamba kugula chimanga kwa alimi. A Mawindo adachenjeza kuti kuchedwaku kwapereka mwayi kwa a malonda ena kudyera alimi masuku pa mutu, komanso kulimbikitsa mchitidwe wozembetsa chimanga kupita ku maiko oyandikana nawo a Mozambique ndi Zambia kumene akuchigulitsa pa mitengo yokwera.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • July 27, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope