Khonsolo ya boma la Nsanje kudzera ku nthambi yoona za ulimi wa ziweto yati yapereka katemera wachigodola, Foot and Mouth Disease, kwa ng’ombe 10 000 pofuna kuziteteza. Mkulu woona za ziweto m’bomalo a Samuel Zuze adati katemerayu yemwe ndi woteteza amupereka ku ma EPA atatu a Makhanga, Magoti ndi Mpatsa. Iwo adati malamulo amati amayenera kubaya zifuyo katemerayu zaka zitatu zilizonse ndipo adzabwerezanso kawiri pakatha miyezi sikisi iliyonse n’chifukwa chake tapanga izi.
“Tiyamikire kulikulu kwathu ku Lilongwe kuunduna wathu wazamalimidwe potithandizira chifukwa tokha sitikanakwanitsa kupeza katemerayu. Tipemphe onse omwe abaitsa katemerayu kuti apitirize kuteteza zifuyo zawo posakadyetsera ku nkhalango zotetezedwa komwe kumakhala njati zomwe zimagawa chigodolachi,” adatero iwo. A Zuze adati kuonjezera kubaya ng’ombezi katemerayu iwo athandizira ng’ombe 615 m’makola 26 kudera la Makhanga EPA komwe kudagwa matenda a zotupa pa thupi la nyama otchedwa Lumpy Skin Disease.
Mmodzi mwa alimi a ziweto a George Chalamba kuchokera m’mudzi mwa Maere T/A Mbenje omwe ali pansi pa Magoti EPA adayamikira chifukwa cha katemerayu. Iwo adati ayesetsa kuti ziweto zawo zisamafike ku malo woteteza ngati ku Matandwe ndi Mwabvi ponena kuti kutero ndi kuika miyoyo ya ziweto pachiopsezo chotenga matenda achigodola. Nawo a William John a m’mudzi wa Kairedze Senior Chief Tengani omwe ali pansi pa Mpatsa EPA adati izi zimachititsa kuti zifuyo zawo zizikhala za thanzi ndipo pa msika zimayenda bwino.
[paywall]
Iwo anati: “Kunena zoona, kwathu kuno ulimi wa za kumunda makamaka zadzinja sizichita bwino ndiye ife timadalira kwambiri ziweto zomwe zimatipatsa zinthu zingapo: ndalama, nyama monga ndiwo komanso mkaka zomwe timathandizidwa kuti tifikire magulu a zakudya onse 6.” Ndipo adaonjeza kupempha kuti khonsolo itsegulire misika yogulitsira ziweto yomwe idalipo kalelo. “Izi zithandizira kuti umbava wa ziweto monga ng’ombe uchepe. Panopa wina aliyense amagulitsa payekhapayekha zomwe zikuthandizira akuba kumaba ziweto zathuzi,” iwo anatero.
[/paywall]
All Zim News – Bringing you the latest news and updates.