Ana 63 mwa 100 akukwapulidwa

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 15 March 2026
📘 Source: MWNation

Makolo ena ati ndi wokondwa ndi mfundo yoti pakhale chilango chokhazikika kwa aphunzitsi amene angapezeke akumenya ophunzira. Komiti yoona za malamulo ku Nyumba ya Malamulo yati iyesetsa kuti pakhale malamulo okhazikika pofuna kuthana ndi mchitidwewu umene umavulaza ana ku thupi ngakhalenso m’maganizo. Makolo amene alankhula ndi atolankhani athu a m’maboma akukondwera ndi ganizoli.

Mmodzi mwa makolowo, a Sosten Kalimanjira a m’mudzi mwa Tawe kwa T/A Kaphuka m’boma la Dedza adati chilango chomenya ana si choyenera. “Zoonadi pakhale malamulo okhwima chifukwa pena zimanyanya. Aphunzitsi ena amamenya ana ngati akumenyana ndi munthu wa msinkhu wawo,” adatero iwo.

Ndipo a Gerald Masitala a m’dera la Mikongo ku Mangochi ati ana ena amaopa kupita kusukulu chifukwa choopa kumenyedwa ndi aphunzitsi. “Kubwera kwa malamulo kuthandiza chifukwa aphunzitsiwo azilangidwa pa sukulupo. Nthawi zina makolo amaopa kukadzudzula aphunzitsi amene ali ndi mbiri yomenya ana chifukwa akatero ena amawalanga anawo powalepheretsa,” adatero iwo.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Koma a Steven Dafter ochokera ku Makande m’boma la Thyolo adati pamene mwana walakwitsa, makolo kapena aphunzitsi ayenera kumukwapula ndithu. Iwo adati: “Ngakhale malemba oyera amaneneratu kuti kholo limene silikwapula mwana limachititsa kuti apulukire. Maufuluwa tikufika nawo penatu!” Wapampando wa komiti yoona za malamuloyo a Gilbert Khonyongwa adati ayesetsa kuti malamulo okhudza aphunzitsi amene amamenya ana.

Iwo adanena izi atakumana ndi bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lomwe lidati ana 63 mwa 100 alionse amalandira chilango chomenyedwa ku sukulu. Bungwelo lati ana ena afapo kaamba komenyedwa ndi aphunzitsi. “Tikambirana ndi anthu athu za kuipa kwa chilango chotere, uku tikusanthula kuti pakhale malamulo okhwina kuti ana athu akhale otetezedwa,” atero iwo.

A Khonyongwa adati komiti yawo ili ndi chidwi chosanthula momwe malamulo alili pano ndi kuona pamene pali banga ndipo aonetsetsa kuti malamulo astopano asapsinje ufulu wa anawo. Mmodzi mwa makomishonala a MHRC a Boniface Massa adati chilango chomenya ana chimachitikabe m’sukulu, makomo ndi nyumba zosamalira ana. “Ili ndi vuto lalikulu zedi. Kafukufuku wathu komanso kaundula wa ofesi yoonketsa zinthu ya National Statistical Office akusonyeza kuti ana akumenyedwa n’kuvulazidwa kapena kuphedwa kumene,” adatero iwo.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • March 15, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope