A Malawi akuti bola Chakwera, DPP yawakhaulitsa – Kabwila

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 10 June 2026
📘 Source: Malawi 24

…wati nthawi yawo zinthu sizinavute ngati pano…Woyankhulira chipani chotsutsa boma cha Malawi Congress, Jessie Kabwila wati a Malawi atopa kale ndi boma la Democratic Progressive ndipo akufunitsitsa a Lazarus Chakwera abwerereso m’boma zomwe wati zichitika mu 2030.Kabwila walankhula izi mu pologaramu ina pa wayilesi ya Zodiak momwe walavulira zakukhosi chipani cha DPP chomwe akuti chikulephera kuyendetsa boma bwino chipambanireni chisankho pa 16 September, 2025.Mwazina, Kabwila waloza chala DPP pakukwera mitengo kwa katundu osiyanasiyana kuphatikizapo mafuta agalimoto, misonkho yochuluka, kulephera kupanga ziganizo zabwino pa zinthu zina komaso kulowa pansi kwa chitetezo m’dziko muno.“Boma iri likupanga chili chonse chothekera kuti a Malawi avutike. Kusatha kwa anthu awawa nkowawa,” watelo Kabwila. “Ndikupempha a boma la DPP, avereni chisoni a Malawi, misonkho mwawonjeza, a Malawi akuvutika ndi misonkho.”Iye wati ngati chipani cha DPP sichisintha kayendetsedwe ka boma, kukhala kosavuta chipani chawo kubwerera m’boma 2030.“Panopa mutati muone m’mene Malawi aliri, aliyese akungoti bola Chakwera &,” wateloso Kabwila.

“Ifeyo tikuwathokoza a DPP kuti akutipangira kampeni. A Malawi ndi amene atiike ife m’boma 2030 uno. 2030 ikuyamba pano.

Sitikukaikiraso, tikubwerera m’boma, nkhani ndi m’mene akuyendetsera zinthu awawa. M’malawi watopa, DPP yawakwana osati masewera.”Kabwila wadzudzulaso chipani cha DPP pomaloza chala chipani chawo kuti ndicho gwero la mavuto azachuma omwe dziko lino likudutsa pano.“Awa analirira ija amati nyanga yasatsi, tinawasemera ndiimeneyi nde lero asamati akamaphunthwa adziyang’ana MCP. Anthuwa asamati vuto ndi ife, kodi mesa iwowa adabetchera kuti amatha?” wafusa Kabwila.Iye adavomereza kuti nthawi yawo zinthu zina sizinali bwino koma wati sizinafike pomwe zafika pano, ndipo wati zinthu zinavuta chifukwa cha mavuto ngati Covid-19, namondwe komaso nkhondo ya dziko la Russia ndi Ukraine.“Inde kunali kulakwitsa nthawi yathu koma sindikukhulupilira kuti kulakwitsa kwathu kungafanane ndikomwe akupanga anzathuwa,” wateloso Kabwila.Pakadali pano, iye wati chipani chawo motsogozedwa ndi a Chakwera chiri kalikiriki kukoza apo ndi apo kuti akatengaso boma mu 2030, asadzatulutsidweso This site uses Akismet to reduce spam.Learn how your comment data is processed.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on Malawi 24

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

📰 Article Attribution
Originally published by Malawi 24 • June 10, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope