A Napoleon Dzombe, omwe alengeza kuti akhazikitsa fakitale yopanga fetereza kufupi ndi hotela yawo ya Kalipano m’boma la Dowa, ati iwo ndi wokonzeka kukwaniritsa izi chifukwa zipangizo zopangira feterezayo zambiri zizichokera m’dziko momwe muno. Iwo ati zipangizo ziwiri, zinki ndi potashi ndizo aziitanitsa kunja kwa dziko lino pomwe Kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya dziko lino, fakitale yopanga fetereza ikhala ikuyamba kupanga feterezayu m’dziko lino mu April chaka cha mawa. A Dzombe ati zomangamanga zonse zili m’chimake ndipo pofika mu April chaka cha mawa, fakitaleyi idzakhala itayamba kupanga feterezayu.
Iwo ati fakitaleyi ili ndi kuthekera kopanga matani 30 kufikira 40 a fetereza pa ola limodzi. “Ndipo titati tigwire ntchito kwa masiku 150 tikhoza kukwanitsa kupanga feteleza wa NPK wa dziko lonse la Malawi,” iwo atero. Pakadalipano, iwo ati ntchito yozika zitsulo za fakitaleyi yomwe idagwira ndi kampani ya zomangamanga ya ku China inatha ndipo kumanganso makoma a fakitaleyi kunathanso.
“Matabwa a denga akonzedwa kale komanso malata tikuwagula kale. Kotero tikuyembekeza kuti ikamafika January chaka cha mawa tikhala titamaliza ntchito yomangamangayi,” iwo atero. A Dzombe, omwenso ndi mwini wake wa Hotelo ya Kalipano m’bomalo adaonjezera kuti: “Pomwe ntchitoyi izidzatha mwezi wa mawa, tiyamba kusonkhanitsa zipangizo zopangira feterezayu ndipo tikuganizira kuti pofika April tikhoza kuyamba kumupanga.” Iwo adaonjezera kuti zipangizo zopitirira theka zopangira feterezayu monga lime, dothi logwirana (clay soil), phosphate komanso malasha zizikhala zikuchokera m’dziko lino ndipo zochepa chabe ziziyitanitsidwa kuchokera ku maiko a kunja.
[paywall]
Iwo ati wina mwa mitundu ya fetereza yemwe fakitaleyi izikhala ikupanga ndi monga NPK, CAN komanso D Compound. Mmodzi mwa akatswiri a za ulimi m’dziko lino a Tamani Nkhono-Mvula ayamikira ntchitoyi yomwe ati yakhala ikunenedwa kwa nthawi yaitali. “Ntchitoyi ndi yabwino kwambiri chifufwa ithandiza kuonetsetsa kuti fetereza akupezeka m’dziko muno mu nthawi yabwino chifukwa nthawi zambiri kuitanitsa feterezayu kuchokera ku maiko akunja kwakhala kukakumana ndi mavuto osiyanasiyana,” iwo atero. Ndipo ati kumangidwa kwa fakitaleyi kuthandizira kuthana ndi mavuto osiyanasiyana omwe amakhalapo maka kuti feterezayu adzafike m’dziko lino ndipo alimi azikhala atapeza feterezayu mu nthawi yabwino.
[/paywall]