Oyimbira watiwonongera masewero – MkandawireÂ

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 02 June 2026
📘 Source: Malawi 24

M’mphuzitsi wa timu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wadandaula kuti kugonja kwake koyamba mu mpikisano wa chaka chino wa FDH Premiership mmanja mwa Karonga United kwadza kamba kakulephera ntchito kwa oyimbira. Mmene imapita mmasewerowa, panali patadutsa masewero asanu koma osagonja koma lero yachinyitsa kumapeto kwenikweni kuti Karonga United ipambane 1-0. Mkandawire anati m’masewero onse, oyimbira wakhala akuthandizira Karonga kuti ipambane.

“Aliyense wawona m’mene woyimbira wachitira, sindinena zambiri koma osewera athu nawonso ndi anthu. Ngakhale Karonga yachinya chigoli chabwino koma oyimbira anayesetsa kuti apeze chigoli” anatero Mkandawire. Red Lions ili pa nambala 7 ndi mapoint okwana 9 pamasewero 6.

Kumbali ya Karonga, chipambano cha lero chomwe adalira chigoli chokhacho cha Godfrey Sibale, chawatengera pa nambala 8 ndi mapoint 8 pamasewero 6. Zateremu ndiye kuti Karonga United yapambana koyamba pakwawo italephera kutero m’masewero awiri omwe yasewerapo This site uses Akismet to reduce spam.Learn how your comment data is processed.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on Malawi 24

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

📰 Article Attribution
Originally published by Malawi 24 • June 02, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope