Amalawi akufinyika

Apr 4, 2026
Amalawi akufinyika

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 04 April 2026
📘 Source: MWNation

Pamene mtengo wa mafuta udakwera Lachitatu sabata ikuthayi, Amalawi ochokera m’madera osiyanasiyana m’dziko lino ati kulira n’kosayamba. Koma ikakuona litsiro mvula siyikata, ochita bizinesi zing’onozing’ono ena amene tacheza nawo m’maboma a Karonga, Ntcheu, Chikwawa, Salima ndi Blantyre ati ngakhale mayendedwe akwera, akulephera kukweza katundu wawo, poopa kuti ogula anyanyala. Pa 1 April, nthambi yoona za mphamvu ya Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) idalengeza kuti mtengo wa petulo udakwera kuchoka pa K4 965 pa lita kufika pa K6 672 pomwe dizilo adachoka pa K4 945 kufika pa K6 687 pa lita ndipo parafini adachoka pa K3 200 kufika pa K5 824.

Mawu a Amalawiwo akupherezera zomwe akuluakulu a mabungwe osiyanasiyana monga loona za ogula la Consumers Association of Malawi (Cama), la eni galimoto zonyamula katundu la Transportation of Malawi ndi ena adauza nyuzipepala yaThe NationLachinayilo kuti kukwera mtengo kwa mafuta kufinya Amalawi. Mayi Ezelina Milanzi, omwe amaoda zovala ku Kyera m’dziko la Tanzania ndi kukagulitsa pa boma la Karonga adati kukwera kwa mafutawa kwachititsa kuti phindu lawo litsike chifukwa amalipira K20 000 kupita ku Songwe ndi kubwerera koma pano ulendowo uli pa K30 000. “Timayenda kamodzi kapena kawiri pa sabata kupita ku Tanzania.

Ulendo wochoka pa Songwe kupita ku Kyera si umavuta chifukwa timagwiritsa ntchito mashiling’i a kumeneko. Pa katundu wa K100 000 timapeza phindu la K30 000. “Apa sitingachitire mwina koma kukweza mitengo kuti phindu lizioneka.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Tsoka ndi ilo, kukweza msanga kumathamangitsa makasitomala chifukwa amanyinyirika chifukwa nawonso akufinyika,” atero iwo. A Joseph Mwasangwale, omwe amayendetsa galimoto ya Sienta ku Karonga komweko ati akumvetsetsa kuti kukwera mtengo kwa mafuta si vuto la dziko lino koma kumene mafutawo amachokera. Iwo ati chachikulu mafutawa azipezeka, alibe nazo vuto.

“Ngakhale atafika K10 000 koma azipezeka pa msika kusiyana n’kuti tizigula kwa anzathu pa mtengo wokwera kwambiri. Iyiyi ndiye imadula kwambiri ndipo anthu amatidandaula popeza dalaivala aliyense amakweza mtengo mmene wafunira,” adatero iwo. Ndipo a Hawker Banda, omwe amaotcha tchipisi pa msika wa njala pafupi ndi chipatala chachikulu cha Ntcheu, ati akaoda thumba limodzi laling’ono pa mtengo wa K180 000, amalipira K2 000 pa thumba kuchokera ku Tsangano.

“Ndi kukwera mtengo wa mafuta akweza kufika pa K3 000 thumba lililonse. Izi zidya phindu limene ndimapeza. Ngakhale kunja kwacha ndipo mbatatesi zilipo zambiri, ndikuona kuti tikakweza msanga kuchoka pa K2 000 mbale imodzi tithamangitsa makasitomala ndiye tizingopereka momwe zikukhaliramu,” atero iwo.

Nkhawa yawo ndi yoti zinthu zina zimene amagwiritsa ntchito pa bizinesi yawoyi monga kabichi, tomato sosi, tsabola, tomato, anyezi ndi mafuta ophikira nazo zikhonza kukwera mtengo. Ndipo a Jackson Kasinja omwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya pulaimale Yambe ku zoni ya Nakondwa makilomita a pakati pa 15 ndi 20 m’boma la Salima a ndipo adati amalipira K12 000 pa njinga ya kabaza koma dzanalo adalipira K28 000. “Mayendedwe akukhala chipsinjo zedi zimene zikukhudza umoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Akadatiganizira kuti boma likambirane ndi okhudzidwa kuti mayendedwe abwerere m’chimake,” adatero iwo.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • April 04, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope