Afufuza zogulitsa Amaryllis Hotel

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 14 March 2026
📘 Source: MWNation

Nyumba ya Malamulo Lachiwiri lidayamba kufufuza momwe oyendetsa thumba la ndalama za penshoni za ogwira ntchito m’boma idagulira hotela ya Amaryllis mu mzinda wa Blantyre pa mtengo wa K128.7 biliyioni. Thumba la PSPTF lidagula hotelayo pa mtengo wa K128.7 biliyoni, ngakhale akadaulo mu 2023 adati mtengo wa hotelayo ndi K30 biliyoni malinga ndi a FDH Bank omwe adayeza hotelayo. M’chaka cha 2024, banki ya CDH Investment Bank idati mtengo wa hotelayo ndi K36.7 biliyoni.

Mmodzi mwa akuluakulu a FDH Bank a Noel Mkulichi adati bankiyo idagwira ntchito yopeza mtengo wa hotelayo itafunsidwa ndi a Nico Assets Manager. “Lipoti lathu lidasonyeza kuti bankiyo ili pa K30 biliyoni chifukwa tidapeza kuti imayenera kukhala pakati pa K25 biliyoni ndi K35 biliyoni. Sitikudziwa kuti ena adayeza hotela yomweyo ndi kupeza kuti ili pa K40 biliyoni,” adatero iwo.

Mkulu wa CDH, Mayi Gillian Kachikondo adati kampani yawo idapeza kuti mtengo wa hotelayo mu 2024 idali pa K36.7 biliyoni. Ndipo popereka umboni ku komiti ya Nyumba ya Malamulo yoona za chuma ya PAC, mkulu wa kampani ya EMJ Advisory a Emmanuel Chisale adati adapeza kuti mtengo wa hotelayo udali pakati pa K115 biliyoni ndi K145 biliyoni, n’chifukwa chake adauika pa K128 biliyoni, imene PSPTF idavomera kugula hotelayo. Nayo kampani ya Nico Asset Managers idati idaika mtengo wa K48 biliyoni koma siyidagwirizane ndi ganizo logula hotelayo chifukwa idalibe phindu lenileni.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

Bungwe la oimira anthu pa milandu, kupyolera mwa wachiwiri kwa mtsogoleri wawo a McHarven Ngwata, lidapereka umboni wake. “Tidakali mkati mofufuza momwe zidakhalira ndiye pakadalipano sitinganene maganizo athu okhazikika,” adatero iwo. Wapampando wa PAC a Steven Baba Marondera adati kafukufukuyu ndi wofunika chifukwa ndi udindo wa Nyumba ya Malamulo kuti ndalama zoposa K1 triliyoni zimene zili m’thumba la mapenshoni a ogwira ntchito m’boma.

“Tikudabwa kuti mwezi wa November kudachitika zambiri zokhudza kugula hotelayi. Ndalama za nkhaninkhani zidapita ndiye chilungamo chiyenera kubwera poyera. Tikugwiranso ntchito ndi bungwe lothana ndi ziphuphu la ACB kuti atithandizire,” adatero iwo. A Marondera adati ogwira ntchito m’boma atetezedwe ndipo ndalama zawo zizigwira ntchito moyenera osati kusakazidwa kupyolera m’ziganizo za bizinesi zoduka mutu Banki yaikulu ya RBM idaimika PSPTF pa lingaliro lake logula Amaryllis mpaka patakhala kafukufuku wokwanira pa momwe zidayendera.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • March 14, 2026

Powered by
AllZimNews

All Zim News – Bringing you the latest news and updates.

By Hope