Mkulu wa bungwe lolimbikitsa demokalase la Centre for Multiparty Democracy (CMD) a Boniface Chibwana aunikira bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti lipeze njira ina yobweretsera mabaloti kuti chisankho chachibwereza chisasokonekere. Izi zadza pomwe pali vuto la ndege yomwe ikuyenera kubweretsa katundu kuphatikizapo mabaloti kuchokera m’dziko la Dubai komwe MEC idapeza kampani yopanga mabalotiwo. Nthambi yoona za maulendo a pa ndege adati ndege yomwe imabweretsa katundu kuchoka ku Dubai idalephera kufika Loweruka kaamba ka nkhondo ya pakati pa Iran, America ndi Israel.
Lolemba sabata inayo pa 17 March 2026, bungwe la MEC likuyembekezeka kudzapangitsa zisankho zachibwereza za aphungu m’madera anayi ndi makhansala m’madera 9. Zokonzekera zambiri zidachitika kale kuphatikizapo kuti omwe akufuna kudzapikisana nawo pa mipando adapereka kale kalata zawo zakhumbo ndipo kampeni ikupita ku mapeto. A Chibwana aunikira kuti anthu m’madera momwe mudzachitike chisankho adikira kwanthawi yaitali ndipo ndi ufulu wawo kusankha owayimilira choncho kuchedwetsa zisankhozo n’kosakomera demokalase.
“Zisankho zomwe tikuyembekezerazi nzothamangitsana ndi nthawi, tili mnyengo ya demokalase ndipo anthu akuyenera kusankha owayimilira. Ngati MEC ikuwona kuti mabaloti avuta kubwera kuchoka ku Dubai, nkwabwino apeze kwina kopangitsa,” atero a Chibwana. MEC idapereka ntchito yopanga mabaloti ku kampani ya Al Ghurair Printing and Publishing ya ku Dubai koma mkangano womwe wabuka pakati pa maiko a America, Israel ndi Iran wasokoneza ntchito zambiri kuphatikizapo za maulendo apa ndege mmayiko akwa aluya.
[paywall]
Koma mneneri wa MEC a Sangwani Mwafulirwa ati pasakhale nkhawa iliyonse chifukwa ndege zochokera ku Dubai zikhoza kuyambanso kubwera nthawi iliyonse. “Tsiku la zisankho ndi pa 17 March 2026 ndipo nthawi ikadalipo yoti titha kulandira mabaloti nkupanga zonse zoyenelera mndondomeko yake kuti anthu adzaponye voti patsikulo,” adatero a Mwafulirwa. Iwo adati bungwe la MEC lilibe malingaliro aliwonse kapena chikonzero chosintha tsiku lazisankho chifukwa ndondomeko zina zonse zikuyenda bwino.
Pano onse ofuna kudzapikisana nawo pachisankho adapeleka kale kalata zawo kubungwe la MEC ndipo tikunena pano kampeni ikupita kumalecheleche. Malingana ndi mkulu wamgwirizano wamabungwe pansi pa Civil Society Elections Integrity Forum (Cseif) a Benedicto Kondowe, MEC ikuyenera kumasuka nkulengeza nthawi yabwino ngati pali zovuta. Iwo ati nkhani yayikulu pazisankho ngati zimenezi ndi Chilungamo komanso kuchita zinthu poyera kuti anthu asataye chikhulupiliro.
[/paywall]
All Zim News – Bringing you the latest news and updates.