Zaka zisanu chifukwa choba katundu

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 11 January 2026
📘 Source: MWNation

Bwalo la First Grade Magistrate ku Lilongwe, Lachinayi lidagamula Mayi Esther James a zaka 38 kuti akakhale ku ndende kwa zaka 5 atapezeka wolakwa pa mlandu woba katundu osiyanasiyana m’nyumba ya mayi wina ku Area 36. Woimira boma pa milandu, a Sub-Inspector Florence Mlanje, adauza bwalolo kuti maiwo akhala akulowa m’nyumba mwa mayiwo popanda chilolezo ndipo pa tsikulo, atalowa adatengamo zinthu monga mapaketi 10 a shuga, mafuta ophikira, matilesi ndi zitenje. A Mlanje adatinso Lachitatu, pa 7 January, mwini nyumbayo adali pafupi chifukwa adalibe zochita zambiri.

Ndipo posakhalitsa, atafika tsizinamtoleyo, adamupeza mwana wa mayiwo, yemwe ali ndi vuto la ulumali, atagona pa matilesi m’nyumbamo ndipo sanachedwetse koma n’kumuchotsapo namugonetsa pansi. Pamapeto pake, adapezanso mwayi woba matilesiwo. Atakaonekera ku bwalo la milandu, mayi wakubayo adaukana mlandu wothyola nyumba ndi kuba katundu zomwe zidachititsa kuti woimira boma pa milandu abweretse mboni zomwe ndi anthu amene adagula katundu yemwe mayiwo amaba m’nyumbamo.

Atampeza wolakwa, mayiwo adapempha khotilo kuti limuganizire popereka chilango chofewa ponena kuti iye ankachitira izi chifukwa cha mavuto komanso kuti ndi koyamba kuchita zoipazo. Koma woimira boma pa milandu, a Mlanje adatsindika zakufunika kopereka chilango chokhwima kuti likhale phunziro kwa ena oipa mtima ngati mayiwo. M’chigamulo chawo, woweruza mlanduwo, a Imrani Phiri, anagamula kuti mayi wakubawo apite ku ndende komwe akakhaleko zaka zisanu.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • January 11, 2026

Powered by
AllZimNews

By Hope