Mabungwe omwe si aboma ayamikira a Pulezidenti a Peter Mutharika pokana kusainira bilu yofuna kuti aphungu aziyendetsa thumba la chitukuko la CDF kuti likhale lamulo. Mu December chaka chatha, Nyumba ya Malamulo idadutsitsa bilu yomwe cholinga chake chidali choti dzanja la aphungu lizikhala pa thumba la CDF ndipo apitirize kuyendetsa zitukuko za m’madera mwawo. Itadutsa biluyo, padali manong’onong’o ndi kukokanakokana chifukwa magulu ambiri amaona kuti madutsidwe a biluyo amaonetsa kuti aphungu ali ndi nthongo kumanja yomwe akufuna kususa pa CDF.
Pa nthawiyo, mabungwe omwe si aboma adanenetsa kuti apempha mtsogoleri wa dziko linoyu kuti asavomere kusainira kuti biluyo ikhale lamulo monga mwa ndondomeko yake. “Tikudabwa kuti aphungu akukakamira CDF ngakhale kuti khoti lidagamula kuti siikuwakhudza, pamenepa tikuonapo kenakake. Koma poti ngakhale yadutsa, siyingakhale lamulo pokhapokha apulezidenti atasainira ndiye tiwapempha iwo kuti asasainire,” adatero wapampando wa mgwirizano wa mabungwewo a Benedicto Kondowe.
Lachiwiri lapitali, mneneri wa apulezidenti a Mutharika Mayi Catherine Maulidi adalengeza kuti a Mutharika adakana kusainira biluyo mmalo mwake adaipereka m’manja mwa maunduna a za malamulo ndi za chuma kuti apange ndondomeko. Iwo adati a Mutharika adapanga izi pakutsata nkhawa za Amalawi komanso pofuna kuteteza ndalama za CDF zomwe ntchito yake n’kupangira chitukuko chakudera. “Apulezidenti anena momveka bwino kuti chitukuko chisamalephere kaamba ka kusowa ndondomeko.
[paywall]
Ndalama za CDF n’zoyenera kutetezedwa koposa kuti phindu lake lizioneka osati zizingosakazidwa,” adateero a Maulidi. Potsatira izi, mabungwe 13 adatulutsa kalata Lachitatu yoyamikira a Mutharika ndipo adati izi zitseguladi zitseko zopereka mphamvu ku anthu komanso zaonetsa kuti a Mutharika sakulowetsa ndale pa chitukuko. “Apapa zikuonetsa kuti a Mutharika akumva nkhawa za anthu, akutsata malamulo komanso ali ndi malingaliro achitukuko moti ife ndife okondwa ndi okhutira ndizomwe apulezidenti apanga,” idatero kalatayo.
Koma kumathero kwake, kalatayo idaunikira kuti maunduna omwe apatsidwa udindo wopanga ndondomekowo aonetsetse kuti akonza zogwira mtima. Magulu ambiri maso awo ali pa thumba la CDF makamaka momwe adalikwenza kuchoka pa K200 miliyoni kufika pa K5 biliyoni dera la phungu aliyense. Chigamulo cha khoti chaka chatha chidati aphungu asamatenge gawo pa kayendetsedwe ka CDF komanso asamapange nawo mapulani a zitukuko pa khonsolo koma sichidawalande mphamvu zochita kalondolondo wa zitukuko.
Malingana ndi malamulo, ntchito za aphungu ndi kupanga malamulo, kulondoloza momwe boma likuyendetsera chuma ndi kuimirira anthu akudera komwe adasankhidwa. Kuonjezera apo, aphungu amakambirana ndi kuvomereza bajeti ya dziko.
[/paywall]