Mabungwe omenyera ufulu wa anthu alandira ndi manja awiri ganizo la nthambi ya za ndende loika makamera m’ndende ngati njira yokhwimitsira chitetezo koma ati pakhale ndondomeko yotetezera ufulu wa omangidwa. Kwa nthawi, kwakhala kukuchitika umbanda kuchokera m’ndende za dziko lino, pomwe akaidi ena amabera anthu m’njira zosiyanasiyana kudzera pa lamya. Komanso, ndende za dziko lino mumalowa zinthu zina zosaloledwa monga mankhwala ozunguza bongo.
Mneneri wa nthambi ya za ndende a Charles Meke atsimikiza kuti ganizo loika makamera m’ndende lidabwera pofuna kukhwimitsa chitetezo m’ndende. “Choyamba, anthu akuyenera kumvetsetsa kuti ntchito yosintha munthu kuti adzabwerere kwawo ali wosinthika siyingayende ngati munthuyo sakukhala malo otetezeka. “Makamera amenewo cholinga chake n’kufuna kuti tichepetse kulowa kwa zinthu zosavomerezeka m’ndende.
Makamerawo adzaikidwa mmalo momwe tikuona kuti mukhoza kumachitika zosayenera,” adatero a Meke. Iwo adati likulu la nthambiyo lili patsogolo paganizolo ndipo lionetsetsa kuti zitheke koma adati anthu akuyenera kumvetsetsa cholinga chake. Mkulu wa bungwe loona za maufulu a anthu kuphatikizapo a m’ndende la Centre for Human Rights, Advice and Assistance (Chreaa) a Victor Mhango ati ganizolo ndi labwino koma mpofunika kusamala.
[paywall]
“M’ndende m’machitikadi zonyansa zambiri zofunika zipangizo ngati makamera kuti zizidziwika. Koma osaiwala kuti m’ndendemo mulinso maufulu ofunika kutetezedwa,” adatero a Mhango. Iwo adamasula kuti kuika makamera m’ndende sikuphwanya ufulu wa omangidwa koma kagwiritsidwe ntchito ka zomwe makamerawo ajambula komanso malo omwe makamerawo aikidwa.
“Ndi dandaulo lomveka kuti m’ndende m’mofunika chitetezo. N’kosayenera kuika makamera m’malo achinsinsi monga zimbudzi, m’mabafa, kolandilira thandizo la chipatala komanso komwe omangidwa amakumanirana ndi owaimirira pa milandu,” adatero a Mhango. Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe omenyera maufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) a Michael Kaiyatsa ati pakufunika ukadaulo wapamwamba wa kagwiritsidwe ntchito ka makamerawo.
“Tikuyenera kuzindikira kuti ufulu wa munthu sumathera pomangidwa ayi, pa malamulo a dziko lino komanso mgwirizano wa maiko, omangidwa amakhalabe ndi maufulu awo onse. “M’ndende anthu amakhala mozunzika chifukwa cha kuthinana, anthu amavala n’kuvula pa mtetete, amasamba, kugona ndi kudzithandiza pamaso pa anzawo ndiye chisinsi ndi ulemu wawo n’zofunika kuteteza,” adatero a Kaiyatsa. Iwo adati ngakhale kuti m’ndende mumachitika zoipa zambiri, omangidwa ena amakhala osalakwa kotero kuwajambula osasamala kanema wawo zikhoza kuonjezera ululu m’miyoyo yawo.
[/paywall]