Kwangotsala masiku anayi kuti tsiku limene Akhristu amakumbukira kubadwa kwa Yesu Khristu. Kafungo ka mpunga, nyama yootcha, nkhuku yowiritsa ngakhale nkhumba yokazinga m’mafuta Amalawi ena akukamvera apooo, kaamba ka mavuto a za chuma. Pamene nyimbo za Khrisimasi zikuyamba kumveka, mabanja ambiri a ku Malawi akukumana ndi mavuto a za chuma.
Kukwera kwa mitengo ndi kuchepa kwa ndalama kwapangitsa anthu kuganiziranso mmene adzakondwerere. Izi ndi malinga ndi omwe tacheza nawo m’madera ena a dziko lino. Ku msika wa Blantyre, wogulitsa mbatatesi a Willy Kaphela wati nyengo imeneyi mmbuyomu amapha makwacha koma chaka chino ogula akubwera moduladula zimene zingachititse kuti Khrisimasi ingokhala loto basi.
Iwo anati: “Vuto lalikulu ndi mmene ndidzaperekere chakudya kwa ana anga. Akulu tikhoza kupirira, koma ana sangamvetse.” Iwo akuti ngakhale chikondwerero chawo chidzakhala chovuta, ku uzimu chikhulupiriro ndi chakuya. Ku Lilongwe, a Sigere Malisawo a ku Area 25 anati ayamba kuchepetsa zinthu zosafunika zomwe akadagula mmbuyomu monga zovala zatsopano ndi mphatso.
[paywall]
“Tidzasunga zofunika zokha. Nthawi zina umamva ngati wochimwa monga kholo kaamba kosowa, koma izi zidutsa,” adatero iwo. Kuonjeza apo, a Emmanuel Nkhambule omwe amayendetsa taxi ku Mzuzu adati ngakhale kugula ufa wokwanira ndi vuto.
“Tidzangokhala ku nyumba ndi kupemphera kuti zinthu zisinthe,” adatero iwo Komabe, ku Zomba mlimi Isaac Nota anati chisangalalo chawo chidzaonjezeka chifukwa boma lachotsa ndalama za sukulu. “Mmbuyomu zimachepetsa ndalama za zikondwerero, tsopano ndidzagwiritsa ntchito zina pa Khrisimasi,” adatero iwo. Atsogoleri a chipembedzo monga abusa Yotam Msumba akulimbikitsa chiyembekezo ngakhale pa mavuto. Katswiri wa za chuma Donasius Pathera adalangiza: “Pewani ngongole, moyo ukupitiriza pambuyo pa zikondwerero.” Popherezera, mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogula la Cama a John Kapito adati anthu apange bajeti, kupewa kugula mwadzidzidzi ndi kubwereka modzivulaza.
[/paywall]