Sangalalani mosamala

Dec 28, 2025

Zimbabwe News Update

🇿🇼 Published: 28 December 2025
📘 Source: MWNation

Pomwe zisangalalo zili mkati, akadaulo achenjeza kuti kusangalala kopanda bajeti ndiko kumachititsa mwezi wa January kukhala wowawa kwa anthu ochuluka makamaka odalira malipiro a pa mwezi. Zikondwerero za Khrisimasi ndi chaka chatsopano za chaka chino zakumana ndi njala yomwe yakhudza anthu 4 miliyoni ndipo mtengo wa chimanga chomwe n’chakudya chodalirika udakwera. Mkulu wa bungwe la anthu ogula a John Kapito ati kupanda kupanga bajeti yogwirizana ndi kapezedwe ka munthu, chiwerengero cha anthu okhudzidwa ndi njala chikhoza kudzakwera.

Iwo ati pomwe boma ndi magulu ena akugawa chakudya kwa okhudzidwa ndi njala, munthunso akuyenera kukhala ndi bajeti ya chakudya pa khomo. “Kusangalala n’kwabwino pa moyo wa munthu koma tikuyenera kuzindikira nyengo zomwe tikudutsamo. January ndi mwezi wovuta ndi kale chifukwa zofunika zimachuluka,” atero a Kapito.

Mwa zina, mwezi wa January anthu amatangwanika ndi za ulimi komanso fizi. “Mwezi omwe ukubwera kutsogoloku ndi wotangwanitsa kwambiri koma bola tsopano tizingoyang’ana za kumunda ndi momwe boma lachotsera fizi ku sukulu za sekondale,” atero Mayi Sibongile Ngwira a ku Area 25 ku Lilongwe. Pano maphwando ali mkati, maulendo alinso mkati ndipo ngakhale anthu alibe ndalama zogulira mphatso ndi kunjoyera, amalonda akubwekera kuti kwa iwo ndi nyengo yopha makwacha.

📖 Continue Reading
This is a preview of the full article. To read the complete story, click the button below.

Read Full Article on MWNation

AllZimNews aggregates content from various trusted sources to keep you informed.

[paywall]

“Ukasemphana ndi ndalama pano, January ngovuta kuti ukokele chifukwa anthu amakhala atagulira ndalama zawo. Inde sizingafanane ndi momwe zinkakhalira kale komabe kangachepe kamapezeka,” adatero a William Benala ku Lilongwe. Koma kadaulo wina pa za chuma wati choyenera kulingalira nchakuti zomwe munthu adzale pano nzomwe adzakolole kuyamba January n’kumalowa mkati mwa chaka.

“Tikakomedwa ndi kusangalala kuyiwala mawa, tidzadutsa ndi zokhoma January chifukwa zomwe tikubzala lero n’zomwe tidzakolole ndiye anthu akondwere koma asayiwale za mtsogolo,” adatero iwo. Iwo achenjeza zodalira ngongole kaamba kolephera kukonzekera moyenera ndipo ati mpofunika kuguliratu katundu wofunikira nkusunga ndalama zikadalipo kuopa kudzaonekera mtsogolo.

[/paywall]

📰 Article Attribution
Originally published by MWNation • December 28, 2025

Powered by
AllZimNews

By Hope